1 Samuel 30:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adakafika kwa anthu 200 otopa kwambiri ndi osathanso kuyenda aja, amene adaaŵasiya ku mtsinje wa Besori. Iwo adanyamuka napita kukakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye aja. Davide adaŵayandikira naŵalonjera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anaturuka kucingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.