1 Samuel 30:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthu ena oipa mtima ndi opandapake a m'gulu la amene adaapita ndi Davide aja, adati, “Chifukwa chakuti sadapite nafe, sitiŵapatsako zofunkha zimene talanditsazi, kungopatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake, ndipo achoke.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pace a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wace ndi ana ace, kuti acoke nao namuke.