1 Samuel 30:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Davide adaŵauza kuti, “Musachite choncho, abale anga, ndi zinthu zimene Chauta watipatsa. Chautayo watisunga ndi kupereka m'manja mwathu gulu lankhondo limene lidabwera kudzamenyana nafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.