1 Samuel 30:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide ndi anthu ake atafika kumzindako adaupeza utapsa, ndipo akazi ao ndi ana anali atatengedwa ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Davide ndi anthu ace anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao amuna ndi akazi anatengedwa ukapolo.