1 Samuel 30:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adapempha nzeru kwa Chauta nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondo la Aamaleke? Kodi ndidzaŵapambana?” Chauta adamuyankha kuti, “Litsatire, pakuti udzalipambana ndithu ndipo udzaŵapulumutsa akapolowo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?” Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Lonriola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.