1 Samuel 31:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
amuna ena olimba mtima adanyamuka, ndipo adayenda usiku wonse, nakachotsa mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake ku khoma la Beteseani. Atabwerera ku Yabesi adatentha mitemboyo kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngwazi zonse zinanyamuka ndi kucezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Sauli, ndi mitembo ya ana ace, pa linga la Betisani; nafika ku Jabezi Gileadi naitentha kumeneko.