1 Samuel 31:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke ndi kundipha.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Sauli ananena ndi wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka, Koma woo nyamula zida zace anakana; cifukwa anaopa ndithu. Cifukwa cace Sauli anatenga lupanga lace naligwera.