1 Samuel 31:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele amene anali tsidya lina la chigwa cha Yezireele, ndiponso amene anali tsidya lina la Yordani, ataona kuti anzao adathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake adafa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Aisrayeli akukhala tsidya lina la cigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordano, anaona kuti Aisrayeli alikuthawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.