1 Samuel 31:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake atatu pa phiri la Gilibowa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'mawa mwace, pakubwera Afilisti kubvula akufawo, anapeza Sauli ndi ana ace atatu ali akufa m'phiri la Giliboa.