1 Samuel 31:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadula mutu wace, natenga zida zace, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira ku nyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.