1 Samuel 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina wa fuko la Benjamini adathaŵa kunkhondoko nakafika ku Silo tsiku lomwelo. Anali atang'amba zovala zake ndi kudzithira dothi kumutu, kuwonetsa chisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wa pfuko la Benjamini anathamanga kucokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace.