1 Samuel 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika, adapeza Eli atakhala pa mpando pambali pa mseu akungoyang'ana, poti ankadera nkhaŵa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene Mbenjamini uja adaloŵa mumzindamo, nayamba kusimba zimene zidaachitika kunkhondoko, anthu onse amumzinda adalira kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.