1 Samuel 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo nkuti Eli ali nkhalamba ya zaka 98, maso ake atachita khungu, kotero kuti sankathanso kupenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ace anangokhala tong'o osapenya,