1 Samuel 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adauza Eli kuti, “Ine ndine amene ndachoka ku nkhondo. Ndathaŵa kumeneko lero lomwe.” Eli adamufunsa kuti, “Nanga nkhondo yayenda bwanji, mwana wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.” Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndacokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, a Nkhondoyo idatani, mwana wanga?