1 Samuel 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adayankha kuti, “Aisraele athaŵa Afilisti ndipo anthu ophedwa pakati pathu ngambirimbiri. Ana anu onse aŵiri aja, Hofeni ndi Finehasi, aphedwa, nalonso Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Aisraeli athawa pamaso pa Afilisti. Anthu ambirimbiri aphedwa. Ana anunso Hofini ndi Finehasi aphedwa. Bokosi la Mulungu nalonso lalandidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, lsrayeli anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukuru kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Pinehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandiwa.