1 Samuel 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adangotchula za Bokosi lachipangano la Chauta, Eli adagwa chankhongo, kuchoka pa mpando wake pafupi ndi chipata. Adathyoka khosi naafa, poti adaali wokalamba ndiponso wonenepa kwambiri. Anali atatsogolera Aisraele zaka makumi anai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangotchula Bokosi la Yehova, Eli anagwa chagada, kuchoka pa mpando wake umene unali mʼmbali mwa chitseko cha mpanda. Khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali okalamba ndi onenepa kwambiri. Iye anatsogolera Israeli zaka makumi anayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa cambuyo pa mpando wace pam bali pa cipata, ndi khosi lace linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkuru thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israyeli zaka makumi anai.