1 Samuel 4:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali ndi pathupi ndipo anali pafupi kuchira. Pamene adamva zakuti Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa, ndiponso kuti Eli, mpongozi wake, pamodzi ndi mwamuna wake adafa, zoŵaŵa za pobala mwana zidamfikira mwadzidzidzi, mwana nkumabadwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mpongozi wace, mkazi wa Pinehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yace yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wace, ndi mwamuna wace anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kucira kwace kwamdzera.