1 Samuel 4:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti mkaziyo anali pafupi kufa, akazi omuthandiza adamuuza kuti, “Limba mtima, wabala mwana wamwamuna.” Koma iye sadayankhe ngakhale kusamalako ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankha, kapena kusamalira.