1 Samuel 4:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwanayo adamutchula dzina loti Ikabodi, ndiye kuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele!” Adatero chifukwa chakuti Bokosi lachipangano la Mulungu linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha imfa ya Eli mpongozi wake ndi ya mwamuna wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anamucha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi cifukwa ca mpongozi wace ndi mwamuna wace.