1 Samuel 4:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene magulu ankhondo adafika ku zithando, atsogoleri a Aisraele adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani Chauta walola kuti Afilisti atigonjetse? Tiyeni tikatenge Bokosi lachipangano la Chauta ku Silo, kuti Chautayo abwere pakati pathu ndipo atipulumutse kwa adani athu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akuru a Israyeli anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la cipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.