1 Samuel 4:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Bokosi lachipangano la Chauta lidafika kuzithandoko, Aisraele onse adayamba kufuula kwambiri, kotero kuti nthaka idagwedezeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakufika likasalo la cipangano la Yehova kuzithando, Aisrayeli onse anapfuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linacita cibvomezi.