1 Samuel 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti atamva phokoso la kufuulako adati, “Kodi kufuula kwakukulu kotere ku zithando za Ahebriku nkwa chiyani?” Atamva kuti Bokosi lachipangano la Chauta lafika kuzithandoko,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?” Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kupfuula kwao, anati, Phokoso ili la kupfuula kwakukuru ku zithando za Aisrayeli litani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidzafika ku zithandozo.