1 Samuel 5:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adatumiza Bokosi lachipanganolo ku Ekeroni. Koma litangofika ku Ekeroniko, anthu akumeneko adalira kuti, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele, abwera nalo kwathu kuno, kuti atiphetse ife pamodzi ndi anthu athu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni. Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anatumiza likasa la Mulungu ku Ekroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekroni, a ku Ekroni anapfuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israyeli, kutipha ife ndi ana athu.