1 Samuel 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake adaitananso akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, ndipo adati, “Chotsani Bokosili, ndipo mulibwezere kumene lidachokera, kuti lingatiphe ife pamodzi ndi anthu athu.” Pakuti munali mantha aakulu zedi mumzinda monsemo. Mulungu ankaŵalanga koopsa anthu akumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mudzi monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Cotsani likasa la Mulungu wa Israyeli, lipitenso kumalo kwace, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mudzi monse; dzanja la Mulungu linabvutadi pamenepo.