1 Samuel 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma m'maŵa mwakenso atadzuka, adangoonanso Dagoni uja atagwa, ali chafufumimba, patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Mutu wa Dagoni ndi manja ake omwe zinali zitaduka ndi kugwera pa chiwundo. Thunthu lake lokha la Dagoniyo ndilo limene lidamutsalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wace ndi zikhato zonse ziwiri za manja ace zinagona zoduka paciundo; Dagoni anatsala thupi lokha.