1 Samuel 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Chauta adalanga koopsa anthu a ku Asidodi. Iwowo pamodzi ndi anthu a m'dziko lozungulira adaŵalanga ndi mafundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'milaga yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova anabvuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lace, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'miraga yace.