1 Samuel 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo ataona m'mene zinthu zinaliri, adati, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele lisakhale ndi ife, pakuti Mulungu wao watilanga kwambiri ifeyo ndi mulungu wathu yemwe Dagoni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti ncomweco, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israyeli lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lace litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.