1 Samuel 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adaitana akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, nafunsana kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipangano la Chauta wa Aisraele?” Anthuwo adayankha kuti, “Bokosi limeneli litumizidwe ku Gati.” Motero adatumiza Bokosi lachipanganolo kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anawafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu wa Israeli tichite nalo chiyani?” Iwo anayankha kuti, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lipite ku Gati.” Kotero analichotsa Bokosi la Mulungu wa Israelilo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati, Ticite nalo ciani likasa la Mulungu wa Israyeli? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati, Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israyeli, napita nalo kumeneko.