1 Samuel 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atafika nalo ku Gati, Chauta adauvuta mzindawo, ndipo anthu adachita mantha kwambiri. Choncho anthu amumzindamo adazunzika kwabasi, ana ndi akulu omwe, kotero kuti mafundo ankaŵatuluka anthu onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akulu ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.