1 Samuel 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi anali atatsitsa Bokosi lachipangano la Chauta ndi bokosi lina lija la pambali pake m'mene munali zinthu zagolide, naŵaika pa mwala waukuluwo. Ndipo anthu a ku Betesemesi adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina kwa Chauta pa tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pa mwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolidi, naziika pa mwala waukuruwo; ndipo anthu a ku Betisemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.