1 Samuel 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nazonso zifanizo zagolide za mbeŵa adazipereka moŵerengetsa mizinda yonse ya Afilisti imene inali ya akalonga asanu aja. Ina inali mizinda yamalinga, ina inali midzi yapamtetete. Mwala waukulu uja umene adaikapo Bokosi lachipangano lija m'munda wa Yoswa ku Betesemesi, udakalipo mpaka pano ngati mboni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumilaga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiponso mbewa zagolidi, monga ciwerengo ca midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumiraga; kufikira ku mwala waukuru, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi.