1 Samuel 6:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adaphapo anthu 70 a ku Betesemesi chifukwa choti adaasuzumira m'Bokosi lachipangano, ndipo anzao adalira, popeza kuti Chauta adaapha anthu ambiri pakati pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betisemesi, cifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, cifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe akuru.