1 Samuel 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adatuma amithenga kwa nzika za ku Kiriyati-Yearimu kukanena kuti, “Afilisti abweza Bokosi lachipangano la Chauta. Bwerani kuno, mudzalitenge, kupita nalo kwanuko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriati-yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.