1 Samuel 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthuwo adafunsa kuti, “Kodi nsembe yopepesera machimoyo idzakhale ya mtundu wanji?” Iwo adayankha kuti, “Idzakhale zifanizo zagolide za mafundo asanu ndi za mbeŵa zisanu kuŵerengetsa akalonga asanu a Afilisti, pakuti mliri womwewo unali pa inu nonse ndi pa akalonga anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?” Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yoparamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolidi, ndi mbewa zisanu zagolidi, monga mwa ciwerengo ca mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.