1 Samuel 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mupange zifanizo za mafundo anu aja ndi za mbeŵa zimene zikuwononga m'dziko mwanu, ndipo mulemekeze Mulungu wa Aisraele. Mwina mwake sadzakuvutaninso, inu ndi milungu yanu ndi dziko lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo mucitire ulemu Mulungu wa lsrayeli; kuti kapena adzaleza dzanja lace pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.