1 Samuel 6:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, tengani, nimukonze gareta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli cikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagareta, muzicotsere ana ao kunka nao kwanu;