1 Samuel 6:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mutenge Bokosi lachipanganolo, muliike pa galeta, ndipo pambali pake muikepo bokosi la zinthu zagolide zija zimene mukutumiza kwa Chauta, kuti zikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake muzitaye ng'ombezo ndipo galeta lizipita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m'bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.