1 Samuel 6:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono muziliyang'ana. Likamangopita kulondola kwao kwa Bokosilo mpaka kukafika ku Betesemesi, ndiye kutidi ndi Mulungu wa Aisraele amene adatidzetsera zovuta zazikuluzi. Koma zikapanda kutero, tidzadziŵa kuti sindiye amene adatizunza, zidangochitika mwatsoka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.