1 Samuel 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu a ku Kiriati-yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wace wamwamuna Eleazeri kuti asunge likasa la Yehova.