1 Samuel 7:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Samuele ankapereka nsembe yopsereza ija, Afilisti adasendera pafupi kuti amenyane ndi Aisraele. Koma Chauta adaŵaopsa Afilistiwo ndi mau onga bingu, naŵasokoneza, mwakuti adamwazikana pamaso pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.