1 Samuel 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Samuele adatenga mwala, nauimiritsa pakati pa Mizipa ndi Sene, ndipo adautcha dzina loti Ebenezeri, ndiye kuti “Mwala wachithandizo,” pakuti adati, “Mpaka pano Chauta wakhala akutithandiza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Samueli anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Seni, naucha dzina lace. Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehovaanatithandiza.