1 Samuel 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Afilisti adagonjetsedwa, ndipo sadaloŵenso m'dziko la Aisraele. Chauta ndiye ankalimbana ndi Afilisti nthaŵi yonse Samuele ali moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli. Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco anagonjetsa Afilisti, ndino iwo sanatumphanso malire a Israyeli ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samueli.