1 Samuel 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira tsiku limene Bokosi lachipangano lija lidakhala ku Kiriyati-Yearimu, padapita nthaŵi yaitali ya zaka makumi aŵiri. Ndipo Aisraele onse adadandaulira Chauta kuti aŵathandize.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu m'Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikuru m'Kiriati-yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israyeli linalirira Yehova.