1 Samuel 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Samuele adauza mtundu wonse wa Aisraele kuti, “Ngati mukubwerera kwa Chauta ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Aasitaroti pakati panu, mtima wanu ukhale pa Chauta ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero adzakupulumutsani kwa Afilisti.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli analankhula ndi banja lonse la Israyeli nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, cotsani pakati pa inu milungu yacilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira iye yekha; mukatero, iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.