1 Samuel 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele m'Mizipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lija, nati, Tinacimwira Yehova. Ndipo Samueli anaweruza ana a Israyeli m'Mizipa.