1 Samuel 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Samuele adatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Adapempherera Aisraele kwa Chauta, ndipo Chauta adamuyankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.