1 Samuel 8:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena idzaŵaika kuti akhale olamulira ankhondo chikwi chimodzi kapena makumi asanu. Ndipo ena azidzalima kumunda kwake ndi kumakolola zolima zake, kusula zida zankhondo ndiponso zipangizo za magaleta ankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
idzawaika akhale otsogolera cikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yace, ndi kutema dzinthu zace, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magareta.