1 Samuel 8:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau ameneŵa akuti “Mutipatse mfumu yoti izitilamulira” sadamkondwetse Samuele. Nchifukwa chake Samueleyo adapemphera kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chimenechi sichinakondweretsa Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cimeneci sicinakondweretsa Samueli, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samueli anapemphera kwa Yehova.