1 Samuel 8:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adayankha kuti, “Umvere zonse zimene anthuwo akukuuza. Sakukana iwe koma Ine. Sakufuna kuti ndikhale mfumu yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.