1 Samuel 9:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Saulo adauza mnyamata wakeyo kuti, “Chabwino. Tiye tizipita.” Choncho adapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.